19 Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+
4 Olamulirawo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zikuyendere bwino.+ Koma ngati ukuchita zoipa,+ chita mantha chifukwa sagwira lupanga pachabe, pakuti iye ndi mtumiki wa Mulungu wosonyeza mkwiyo wa Mulungu kwa munthu wochita zoipa.+