22 Ndithu ndidzachititsa nyumba yako kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya, chifukwa chakuti wandikwiyitsa n’kuchimwitsanso Isiraeli.’+
7 Ukaphe anthu a m’nyumba ya mbuye wako Ahabu, kuti ine ndibwezere+ magazi a atumiki anga aneneri ndiponso magazi a atumiki onse a Yehova amene Yezebeli anapha.+
36 Anthuwo atabwerera kwa Yehu kukamuuza, iye anati: “Amenewo ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera+ mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, kuti, ‘M’munda wa ku Yezereeli, agalu adzadya mnofu wa Yezebeli.+