6 Iye anayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ monga mmene ankachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa anakwatira mwana wa Ahabu.+ Ndipo iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+
7 Pajatu ana+ a Ataliya mkazi woipa uja anathyola nyumba ya Mulungu woona,+ n’kutenga zinthu zonse zopatulika+ za m’nyumba ya Yehovayo n’kukazipereka kwa Abaala.”+