2 Mbiri 26:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+ Miyambo 16:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+ Habakuku 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Taona! Iye wadzitukumula+ ndipo si wowongoka mtima. Koma wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.+ Agalatiya 6:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pakuti ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero,+ akudzinyenga. Yakobo 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+
16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+
4 “Taona! Iye wadzitukumula+ ndipo si wowongoka mtima. Koma wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.+
6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+