19 Yosiya anachotsanso akachisi onse+ a m’malo okwezeka amene anali m’mizinda+ ya ku Samariya, amene mafumu+ a Isiraeli anamanga kuti akwiyitse Mulungu.+ Iye anawachitira zofanana ndi zonse zimene anachita ku Beteli.+
30Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembanso makalata ku Efuraimu+ ndi ku Manase,+ kuti abwere kunyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu kudzachita pasika+ kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.