Genesis 26:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Zitatero, Isaki anayamba kubzala mbewu m’dzikomo.+ M’chaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa mbewu zimene anabzala, anakolola zochuluka kuwirikiza nthawi 100,+ popeza Yehova anali kum’dalitsa.+ Deuteronomo 28:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Madalitso onsewa adzakutsata ndi kukupeza+ chifukwa ukumvera mawu a Yehova Mulungu wako: Salimo 5:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pakuti inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama.+Mudzamutchinga ndi chivomerezo chanu+ ngati kuti mukum’teteza ndi chishango chachikulu.+ Salimo 84:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+Iye amatikomera mtima ndi kutipatsa ulemerero.+Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.+ Salimo 128:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+ Miyambo 10:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa,+ ndipo sawonjezerapo ululu.+
12 Zitatero, Isaki anayamba kubzala mbewu m’dzikomo.+ M’chaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa mbewu zimene anabzala, anakolola zochuluka kuwirikiza nthawi 100,+ popeza Yehova anali kum’dalitsa.+
12 Pakuti inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama.+Mudzamutchinga ndi chivomerezo chanu+ ngati kuti mukum’teteza ndi chishango chachikulu.+
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+Iye amatikomera mtima ndi kutipatsa ulemerero.+Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.+
2 Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+