Ekisodo 15:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndipo mu ukulu wanu wopambana mumagwetsa otsutsana nanu.+Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.+ Salimo 1:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma oipa sali choncho.Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.+ Salimo 35:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Akhale ngati mankhusu ouluzika ndi mphepo,+Mngelo wa Yehova awapitikitse.+ Yesaya 17:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Mitundu ya anthu+ idzasokosera ngati mkokomo wa madzi ambiri. Iye adzawadzudzula,+ ndipo iwo adzathawira kutali. Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo m’mapiri ndiponso adzauluzika ngati tizitsotso touluzika ndi mphepo yamkuntho.+ Hoseya 13:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Chotero iwo adzakhala ngati mitambo ya m’mawa+ ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma. Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika kuchokera pamalo opunthira mbewu+ ndiponso ngati utsi umene umatuluka m’chumuni kudenga.* Mateyu 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili m’manja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira m’nkhokwe,+ koma mankhusu adzawatentha+ ndi moto umene sungazimitsidwe.”
7 Ndipo mu ukulu wanu wopambana mumagwetsa otsutsana nanu.+Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.+
13 Mitundu ya anthu+ idzasokosera ngati mkokomo wa madzi ambiri. Iye adzawadzudzula,+ ndipo iwo adzathawira kutali. Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo m’mapiri ndiponso adzauluzika ngati tizitsotso touluzika ndi mphepo yamkuntho.+
3 Chotero iwo adzakhala ngati mitambo ya m’mawa+ ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma. Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika kuchokera pamalo opunthira mbewu+ ndiponso ngati utsi umene umatuluka m’chumuni kudenga.*
12 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili m’manja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira m’nkhokwe,+ koma mankhusu adzawatentha+ ndi moto umene sungazimitsidwe.”