Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikika pamaso pako mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+

  • Salimo 72:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale.+

      Nthawi zonse pamene dzuwa latuluka, dzina lake lizitchuka,

      Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.*+

      Mitundu yonse ya anthu imutche wodala.+

  • Yesaya 11:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Zekariya 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munthu ameneyu adzamanga kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero.+ Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.+ Maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana.+

  • Yohane 12:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Pamenepo khamu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva m’Chilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu adzakwezedwa m’mwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?”+

  • Chivumbulutso 22:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu+ ndi mbadwa+ ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena