Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 60:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 60 “Imirira+ mkazi iwe! Onetsa kuwala kwako,+ pakuti kuwala kwako kwafika,+ ndipo ulemerero wa Yehova wakuunika.+

  • Yesaya 66:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Ndidzachita zinthu zazikulu pakati pawo monga chizindikiro.+ Opulumuka ena ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu,+ ku Tarisi,+ ku Puli, ndi ku Ludi.+ Ndidzawatumiza kwa anthu odziwa kukoka uta ku Tubala ndi ku Yavani.+ Ndidzawatumiza kuzilumba zakutali,+ kwa anthu amene sanamve mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga.+ Iwo adzanenadi za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+

  • Mateyu 28:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse+ kuti akhale ophunzira anga.+ Muziwabatiza+ m’dzina la Atate,+ ndi la Mwana,+ ndi la mzimu woyera,+

  • 1 Petulo 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+

  • Chivumbulutso 14:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga.+ Iye anali ndi uthenga wabwino+ wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena