Salimo 18:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+Makala onyeka anatuluka mwa iye. Salimo 50:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sadzakhala chete.+Pamaso pake pali moto wonyeketsa,+Ndipo pamalo onse omuzungulira pali mkuntho wamphamvu.+ Danieli 7:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Mtsinje wa moto unali kuyenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse,+ ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linakhala pansi, ndipo mabuku anatsegulidwa. Nahumu 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+ Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto+ ndipo miyala idzagwetsedwa chifukwa cha iye. Habakuku 3:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Mliri unali kuyenda patsogolo pake+ ndipo matenda otenthetsa thupi anali kuyenda patsogolo pa mapazi ake.+ Aheberi 12:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Pakuti Mulungu wathu alinso moto wowononga.+
8 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+Makala onyeka anatuluka mwa iye.
3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sadzakhala chete.+Pamaso pake pali moto wonyeketsa,+Ndipo pamalo onse omuzungulira pali mkuntho wamphamvu.+
10 Mtsinje wa moto unali kuyenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse,+ ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linakhala pansi, ndipo mabuku anatsegulidwa.
6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+ Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto+ ndipo miyala idzagwetsedwa chifukwa cha iye.
5 Mliri unali kuyenda patsogolo pake+ ndipo matenda otenthetsa thupi anali kuyenda patsogolo pa mapazi ake.+