Deuteronomo 7:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu+ kuti akulanditseni m’nyumba yaukapolo,+ m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani,+ komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+ Salimo 106:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chotero anawapulumutsa m’manja mwa wodana nawo,+Ndipo anawawombola m’manja mwa mdani.+ Yesaya 35:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+ Yeremiya 15:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Ndidzakulanditsa m’manja mwa anthu oipa+ ndipo ndidzakuwombola m’manja mwa anthu ankhanza.” Mika 4:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu waukulu ngati mkazi amene akumva kupweteka kwambiri pobereka.+ Tsopano uchoka m’tauni ndipo ukakhala kumudzi.+ Ukafika mpaka ku Babulo+ koma kumeneko udzapulumutsidwa.+ Kumeneko Yehova adzakuwombola m’manja mwa adani ako.+ Luka 1:74 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 74 kuti pambuyo pakuti tapulumutsidwa m’manja mwa adani,+ atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye+ mopanda mantha,
8 Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu+ kuti akulanditseni m’nyumba yaukapolo,+ m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani,+ komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+
10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+
10 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu waukulu ngati mkazi amene akumva kupweteka kwambiri pobereka.+ Tsopano uchoka m’tauni ndipo ukakhala kumudzi.+ Ukafika mpaka ku Babulo+ koma kumeneko udzapulumutsidwa.+ Kumeneko Yehova adzakuwombola m’manja mwa adani ako.+
74 kuti pambuyo pakuti tapulumutsidwa m’manja mwa adani,+ atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye+ mopanda mantha,