3 Patapita nthawi, Sauli anafika kumakola a nkhosa amiyala m’mphepete mwa msewu, kumene kunali phanga. Choncho Sauli analowa mmenemo kukadzithandiza.+ Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali atakhala pansi m’zigawo za mkatikati za phangalo,+ kumbuyo kwambiri.