Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu?+

      Ndani angakhale m’phiri lanu lopatulika?+

  • Salimo 27:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova,+

      Chimenecho ndi chimene ndimachikhumba,+

      N’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+

      Kuti ndione ubwino wa Yehova,+

      Komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.+

  • Salimo 65:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu,+

      Kuti akhale m’mabwalo anu.+

      Tidzakhutira ndi zinthu zabwino za m’nyumba yanu,+

      Malo anu oyera kapena kuti kachisi wanu woyera.+

  • Salimo 84:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Odala ndi anthu amene akukhala m’nyumba yanu!+

      Iwo akupitirizabe kukutamandani.+ [Seʹlah.]

  • Salimo 122:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 122 Ndinakondwera pamene anandiuza kuti:+

      “Tiyeni tipite+ kunyumba ya Yehova.”+

  • Luka 2:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Tsopano anali mkazi wamasiye,+ ndipo anali ndi zaka 84 koma sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku,+ anali kusala kudya ndi kupereka mapembedzero.

  • Chivumbulutso 21:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema+ cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo,+ ndipo iwo adzakhala anthu ake.+ Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena