9 Pamapeto pake, Hamani anatuluka tsiku limenelo ali wokondwa+ komanso akusangalala kwambiri mumtima mwake. Koma atangoona Moredekai pachipata cha mfumu+ komanso kuti sanaimirire+ ndi kunthunthumira chifukwa cha iye,+ nthawi yomweyo Hamani anamukwiyira kwambiri+ Moredekai.