Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 19:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Choncho pamene Mulungu anawononga mizinda ya m’Chigawocho, anakumbukira Abulahamu. Anatero mwa kupulumutsa Loti ku chiwonongeko pamene ankawononga mizinda imene Loti anali kukhalako.+

  • Salimo 37:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Pakuti anthu oipa adzatheratu onse,+

      Ndipo adani a Yehova adzafanana ndi busa la msipu wobiriwira mochititsa kaso.

      Iwo adzatha.+ Adzazimiririka ndi kusanduka utsi.+

  • Miyambo 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Chilungamo chimateteza munthu amene sachita zopweteka ena,+ koma wochimwa amawonongedwa ndi zoipa.+

  • Miyambo 14:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Woipa adzakankhidwa chifukwa cha kuipa kwake,+ koma wolungama adzapeza malo othawirako chifukwa cha mtima wake wosagawanika.+

  • 2 Petulo 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndithu, Mulungu sanalekerere angelo+ amene anachimwa aja osawapatsa chilango, koma mwa kuwaponya mu Tatalasi,*+ anawaika m’maenje a mdima wandiweyani powasungira chiweruzo.+

  • 2 Petulo 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 ndipo mwa zimenezi, dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena