Salimo 141:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga.+Ikani wolondera patsogolo pa milomo yanga.+ Miyambo 10:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa,+ koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+ Miyambo 12:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Munthu woipa amakodwa ndi kuchimwa kwa milomo yake,+ koma wolungama amachoka m’masautso.+ Miyambo 13:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Amene amayang’anira pakamwa pake amasunga moyo wake.+ Amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+ Mlaliki 10:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Ngakhale m’chipinda chako, usanenere mfumu zoipa,+ ndipo m’zipinda zimene umagona usanenere zoipa aliyense wolemera,+ chifukwa cholengedwa chouluka chikanena mawu ako ndipo chinachake chokhala ndi mapiko chikaulula zimene wanena.+
19 Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa,+ koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+
3 Amene amayang’anira pakamwa pake amasunga moyo wake.+ Amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+
20 Ngakhale m’chipinda chako, usanenere mfumu zoipa,+ ndipo m’zipinda zimene umagona usanenere zoipa aliyense wolemera,+ chifukwa cholengedwa chouluka chikanena mawu ako ndipo chinachake chokhala ndi mapiko chikaulula zimene wanena.+