Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 10:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa,+ koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+

  • Miyambo 12:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munthu woipa amakodwa ndi kuchimwa kwa milomo yake,+ koma wolungama amachoka m’masautso.+

  • Miyambo 18:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pakamwa pa munthu wopusa m’pamene pamamuwononga,+ ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.+

  • Mateyu 12:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse opanda pake amene iwo amalankhula.+

  • Yakobo 1:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ngati munthu akudziona ngati wopembedza,+ koma salamulira lilime lake,+ ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake,+ kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.+

  • Yakobo 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pakuti lilime timatamanda nalo Yehova,+ amenenso ndi Atate,+ komanso ndi lilime lomwelo timatemberera+ anthu amene analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.”+

  • Yuda 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Anthu amenewa ndi okonda kung’ung’udza,+ okonda kudandaula za moyo wawo, ongotsatira zilakolako zawo,+ ndipo amalankhula modzitukumula.+ Amatamandanso anthu ena+ n’cholinga choti apezepo phindu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena