Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 19:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka,+ ndiponso musamakondere munthu wolemera.+ Mnzako uzimuweruza mwachilungamo.

  • Deuteronomo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Musamakondere poweruza.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope munthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu.+ Mlandu umene wakuvutani muziubweretsa kwa ine kuti ndiumve.’+

  • Deuteronomo 16:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama.

  • 2 Mbiri 19:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Tsopano mantha+ a Yehova akugwireni.+ Samalani mmene mukuchitira+ chifukwa Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo+ kapena watsankho,+ ndipo salandira chiphuphu.”+

  • 1 Timoteyo 5:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu+ ndiponso angelo ochita kusankhidwa, kuti uzitsatira malangizo amenewa popanda kuweruziratu. Usachite kanthu ndi maganizo okondera.+

  • Yakobo 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mumasankhana pakati panu+ ndipo mwakhala oweruza+ opereka zigamulo zoipa,+ si choncho kodi?

  • 1 Petulo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena