Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 10:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Pamene mukubwera kuchihema chokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa,+ kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale,

  • Esitere 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Amtokomawo anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndi lamulo limene linaperekedwa m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Ndipo mfumu ndi Hamani, anakhala pansi kuti amwe vinyo,+ koma mumzinda wa Susani+ munali chipwirikiti.+

  • Mlaliki 10:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Dziko iwe, ndiwe wodala ngati mfumu yako ili mwana wochokera ku banja lachifumu, ndipo akalonga ako amadya pa nthawi yake kuti akhale amphamvu, osati kumangomwa mopitirira muyezo.+

  • Yesaya 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Ansembe ndi aneneri+ asochera chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Asokonezeka chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku+ chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Sakuonanso bwino ndipo zochita zawo zikusonyeza kuti sakuganiza bwino.

  • Danieli 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pakumwa vinyoyo, iwo anali kutamanda milungu yagolide, yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala.+

  • Hoseya 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Dama, vinyo wakale ndi vinyo wotsekemera zimawononga nzeru za munthu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena