Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 31:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Chifukwa angamwe n’kuiwala malamulo ndi kupondereza ufulu wa ana ovutika.+

  • Yesaya 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Ansembe ndi aneneri+ asochera chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Asokonezeka chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku+ chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Sakuonanso bwino ndipo zochita zawo zikusonyeza kuti sakuganiza bwino.

  • Ezekieli 44:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ansembe asamamwe vinyo ngati akukalowa m’bwalo lamkati.+

  • Hoseya 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Dama, vinyo wakale ndi vinyo wotsekemera zimawononga nzeru za munthu.+

  • Aefeso 5:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndiponso, musamaledzere naye vinyo,+ mmene muli makhalidwe oipa,+ koma khalanibe odzaza ndi mzimu.+

  • 1 Timoteyo 3:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,*+ kapena wandewu,+ koma wololera.+ Asakhale waukali,+ kapena wokonda ndalama.+

  • 1 Timoteyo 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Nawonso atumiki othandiza+ akhale opanda chibwana, osanena pawiri, osakonda kumwa vinyo wambiri, ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo.+

  • Tito 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera.+ Pokhala mtumiki*+ wa Mulungu, asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa,*+ wandewu,+ kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena