Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 23:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Ulamuliro wake umakhala ngati kuwala kwa m’mawa pamene dzuwa lawala,+

      M’mawa wopanda mitambo.

      Umakhala ngati msipu womera padziko mvula ikakata, dzuwa n’kuwala.’+

  • Salimo 97:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kuwala kwaunikira wolungama,+

      Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+

  • Salimo 119:105
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,+

      Ndi kuwala kounikira njira yanga.+

  • Danieli 12:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Koma iwe Danieli, sunga mawuwa mwachinsinsi ndipo utseke ndi kumata bukuli+ kufikira nthawi yamapeto.+ Anthu ambiri adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.”+

  • Mateyu 5:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Inu ndinu kuwala kwa dziko.+ Mzinda ukakhala paphiri subisika.

  • 1 Akorinto 13:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pakuti pa nthawi ino sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwinobwino,+ koma pa nthawiyo zidzakhala maso ndi maso.+ Pa nthawi ino zimene ndikudziwa n’zoperewera, koma pa nthawiyo ndidzadziwa bwinobwino ngati mmene ineyo ndikudziwikira bwinobwino.+

  • 2 Akorinto 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti Mulungu ndiye anati: “Kuwala kuunike kuchokera mu mdima,”+ ndipo kudzera mwa nkhope ya Khristu,+ waunika mitima yathu kuti iwale+ ndi ulemerero wokhudzana ndi kudziwa+ Mulungu.

  • 2 Petulo 1:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Choncho mawu aulosiwa+ ndi odalirika kwambiri,+ ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewo ali ngati nyale+ imene ikuwala mu mdima, m’mitima yanu, mpaka m’bandakucha, nthanda*+ ikadzatuluka.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena