Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+

  • Yobu 23:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Sindisiya malamulo otuluka pakamwa pake.+

      Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake+ kuposa zimene akufuna kuti ndichite.

  • Salimo 19:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Chilamulo+ cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa moyo.+

      Zikumbutso+ za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+

  • Salimo 107:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Wanzeru ndani? Iye aona zimenezi,+

      Ndi kuchita chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+

  • Salimo 119:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  34 Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu,+

      Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.+

  • Salimo 119:100
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,+

      Chifukwa ndimasunga malamulo anu.+

  • 2 Timoteyo 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke+ kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena