18 Mmodzi mwa atumikiwo anayankha, kuti: “Inetu ndinaona luso loimba+ la mwana wa Jese wa ku Betelehemu. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso wamphamvu,+ mwamuna wankhondo,+ wolankhula mwanzeru+ ndi wooneka bwino,+ komanso Yehova ali naye.”+
8 Bwana wake uja anamuyamikira mtumiki ameneyu, ngakhale kuti anali wosalungama, chifukwa anachita mwanzeru.+ Pakuti ana a m’dziko lino amachita mwanzeru pochita zinthu ndi anthu a m’badwo wawo kuposa ana a kuwala.+