1 Samueli 15:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Patapita nthawi Samueli anam’peza Sauli, ndipo Sauli anauza Samueli kuti: “Yehova akudalitseni.+ Ndachita zimene Yehova ananena.”+ Salimo 36:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pakuti amadzinyenga yekha,+Ndipo sazindikira cholakwa chake ndi kudana nacho.+ Miyambo 21:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Njira iliyonse ya munthu imaoneka yowongoka m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza mitima.+ Miyambo 30:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pali m’badwo umene umadziona kuti ndi woyera,+ koma sunasambe kuti uchotse ndowe zake.+ Yeremiya 17:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.*+ Ndani angaudziwe? Luka 18:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Mfarisi uja anaimirira+ ndi kuyamba kupemphera+ mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu.+
13 Patapita nthawi Samueli anam’peza Sauli, ndipo Sauli anauza Samueli kuti: “Yehova akudalitseni.+ Ndachita zimene Yehova ananena.”+
9 “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.*+ Ndani angaudziwe?
11 Mfarisi uja anaimirira+ ndi kuyamba kupemphera+ mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu.+