Miyambo 16:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Munthu ndiye amakonza maganizo mumtima mwake,+ koma kwa Yehova n’kumene kumachokera yankho la palilime lake.+ Mlaliki 10:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Mawu a m’kamwa mwa munthu wanzeru amakhala osangalatsa,+ koma milomo ya munthu wopusa imamuwononga.+ Yesaya 57:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 “Ndikulenga chipatso cha milomo.+ Mtendere wosatha udzakhala kwa yemwe ali kutali ndiponso kwa yemwe ali pafupi,+ ndipo ndidzam’chiritsa,”+ akutero Yehova. Aheberi 13:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+
16 Munthu ndiye amakonza maganizo mumtima mwake,+ koma kwa Yehova n’kumene kumachokera yankho la palilime lake.+
12 Mawu a m’kamwa mwa munthu wanzeru amakhala osangalatsa,+ koma milomo ya munthu wopusa imamuwononga.+
19 “Ndikulenga chipatso cha milomo.+ Mtendere wosatha udzakhala kwa yemwe ali kutali ndiponso kwa yemwe ali pafupi,+ ndipo ndidzam’chiritsa,”+ akutero Yehova.
15 Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+