9 Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, pakuti imeneyo ndiyo mphoto yako pamoyo,+ ndi pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano.