Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 25:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anapeza kuti akuchita phwando m’nyumba mwake ngati phwando la mfumu.+ Nabala anali kusangalala kwambiri mumtima mwake ndipo anali ataledzereratu.+ Abigayeli sanamuuze chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu, kufikira m’mawa mwake.

  • Miyambo 21:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Wokonda zosangalatsa adzakhala munthu wosauka.+ Wokonda vinyo ndi mafuta sadzapeza chuma.+

  • Danieli 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndiyeno mfumu Belisazara+ anakonzera nduna zake 1,000 phwando lalikulu, ndipo iyeyo anali kumwa vinyo+ atakhala kutsogolo kwawo.

  • Hoseya 7:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu, akalonga adzidwalitsa+ ndipo ali ndi ukali chifukwa cha vinyo.+ Mfumuyo yatambasula dzanja lake pamodzi ndi anthu onyoza.

  • Maliko 6:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndiyeno tsiku loyenera+ linafika pamene Herode anakonzera chakudya chamadzulo nduna zake, akuluakulu a asilikali ndi atsogoleri a mu Galileya, pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena