Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 65:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iwo amanena kuti, ‘Khala pawekha. Usandiyandikire, kuti ndingakupatsire chiyero changa.’+ Iwo ali ngati utsi m’mphuno mwanga,+ ngati moto woyaka tsiku lonse.+

  • Mateyu 6:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu+ pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni, chifukwa mukatero simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba.

  • Mateyu 12:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Afarisi ataona zimenezi anamuuza kuti:+ “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”+

  • Mateyu 23:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika.+ Kupereka zinthu zimenezi n’kofunikadi, koma osanyalanyaza zinthu zinazo.

  • Luka 18:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Yesu ananenanso fanizo lotsatirali kwa ena odzidalira, odziona ngati olungama+ amenenso amaona ena onse ngati opanda pake.+ Iye anati:

  • Aroma 10:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndipo posadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.+

  • Aroma 14:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Nanga n’chifukwa chiyani umaweruza m’bale wako?+ Kapenanso n’chifukwa chiyani umanyoza m’bale wako? Pakuti tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu+ wa Mulungu.

  • Akolose 2:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi,+ ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena