Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Kodi ungazindikire zinthu zozama za Mulungu,+

      Kapena kodi ungadziwe mapeto a kukula kwa Wamphamvuyonse?

  • Salimo 36:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+

      Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+

      Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+

  • Salimo 139:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+

      Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+

  • Yesaya 55:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Pakuti monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi,+ momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu,+ ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.+

  • Aroma 11:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena