Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 39:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Taonani! Mwachepetsa masiku anga.+

      Ndipo nthawi ya moyo wanga si kanthu pamaso panu.+

      Ndithudi, munthu aliyense ngakhale atakhala wamphamvu bwanji, sali kanthu koma ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ [Seʹlah.]

  • Mlaliki 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse.+ Nditatero, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe ndipo kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+

  • Mlaliki 2:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Munthu wabwino pamaso pa Mulungu,+ Mulunguyo amam’patsa nzeru, kudziwa zinthu, ndi kusangalala.+ Koma wochimwa amam’patsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene ali wabwino pamaso pa Mulungu woona.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo kuli ngati kuthamangitsa mphepo.+

  • Mlaliki 6:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+

  • Luka 12:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena