14 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu+ ndiponso ngati mkango wamphongo kwa nyumba ya Yuda. Ineyo ndidzawakhadzulakhadzula ndekha ndi kuwataya ndipo sipadzakhala wowalanditsa.+
21 Pakuti pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu+ chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano,+ ndipo sichidzachitikanso.