-
Ezekieli 29:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndilanga iwe Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndiwe chilombo chachikulu cha m’nyanja+ chimene chagona m’ngalande zake zotuluka mumtsinje wa Nailo.+ Ndiwe chilombo chimene chanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga, ndipo ineyo ndinaupanga ndekha.’+
-
-
Ezekieli 32:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Farao, mfumu ya Iguputo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Iwe wawonongedwa ngakhale kuti unali ngati mkango wamphamvu pakati pa mitundu ina ya anthu.+
“‘Unali ngati chilombo cham’nyanja.+ Nthawi zonse unali kuyenda mwamphamvu ngati madzi m’mitsinje yako, ndipo unali kuvundula madzi ndi mapazi ako ndi kudetsa mitsinjeyo.’
-