Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Choncho madziwo anabwereradi,+ ndipo anamiza magaleta ankhondo ndi asilikali apamahatchi a magulu onse ankhondo a Farao, amene analondola Aisiraeli m’nyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+

  • Salimo 136:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Amenenso anakutumulira Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira:+

      Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

  • Yesaya 51:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu,+ iwe dzanja la Yehova!+ Dzuka ngati masiku akale, ngati m’mibadwo yakalekale.+ Kodi si iwe amene unaphwanyaphwanya Rahabi,+ amene unabaya* chilombo cha m’nyanja?+

  • Ezekieli 29:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndilanga iwe Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndiwe chilombo chachikulu cha m’nyanja+ chimene chagona m’ngalande zake zotuluka mumtsinje wa Nailo.+ Ndiwe chilombo chimene chanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga, ndipo ineyo ndinaupanga ndekha.’+

  • Ezekieli 32:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Farao, mfumu ya Iguputo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Iwe wawonongedwa ngakhale kuti unali ngati mkango wamphamvu pakati pa mitundu ina ya anthu.+

      “‘Unali ngati chilombo cham’nyanja.+ Nthawi zonse unali kuyenda mwamphamvu ngati madzi m’mitsinje yako, ndipo unali kuvundula madzi ndi mapazi ako ndi kudetsa mitsinjeyo.’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena