15 Ndidzaika+ chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ ndi pakati pa mbewu yako+ ndi mbewu yake.+ Mbewu ya mkaziyo+ idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe+ udzaivulaza chidendene.”+
4 Sudzatchedwanso mkazi wosiyidwa mpaka kalekale+ ndipo dziko lako silidzatchedwanso labwinja.+ Koma iweyo dzina lako lidzakhala “Ndimakondwera Naye,”+ ndipo dziko lako lidzatchedwa “Mkazi Wokwatiwa.” Pakuti Yehova adzakondwera nawe ndipo dziko lako lidzakhala ngati mkazi wokwatiwa.+
27 Pakuti Malemba amati: “Kondwera, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Kuwa ndipo fuula mokondwa, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+