Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mbiri 28:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+

  • Salimo 14:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Koma kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+

      Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+

  • Mateyu 7:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Pakuti aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.

  • Luka 13:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 “Yesetsani+ mwamphamvu kulowa pakhomo lopapatiza.+ Chifukwa ambiri ndikukuuzani, adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha.+

  • Aheberi 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 iye wapatulanso tsiku lina chifukwa wagwiritsa ntchito mawu akuti “Lero” mu salimo la Davide, pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri. Izi zikugwirizana ndi zimene tanena kale zija kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena