Yeremiya 47:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 47 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti.+ Pa nthawiyi, Farao anali asanathire nkhondo mzinda wa Gaza.+ Ezekieli 25:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ ndi kuwononga anthu onse okhala m’mbali mwa nyanja.+ Yoweli 3:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Tsopano ndili nawenso chiyani iwe Turo ndi Sidoni+ ndiponso inu nonse okhala m’chigawo cha Filisitiya?+ Kodi zimenezi ndi zimene mukundipatsa monga mphoto yanga? Ngati mukundipatsa zimenezi, ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+ Amosi 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti Gaza wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anthu onse ogwidwa ukapolo+ anawapereka ku Edomu.+ Zefaniya 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,+ ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+ Kunena za Asidodi,+ anthu ake adzawathamangitsa dzuwa lili paliwombo,+ ndipo Ekironi adzazulidwa.+ Zekariya 9:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha. Gaza adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitikiranso Ekironi+ chifukwa chakuti amene anali kumudalira+ adzachita manyazi. Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu ndipo m’dziko la Asikeloni simudzakhalanso anthu.+
47 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti.+ Pa nthawiyi, Farao anali asanathire nkhondo mzinda wa Gaza.+
16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ ndi kuwononga anthu onse okhala m’mbali mwa nyanja.+
4 “Tsopano ndili nawenso chiyani iwe Turo ndi Sidoni+ ndiponso inu nonse okhala m’chigawo cha Filisitiya?+ Kodi zimenezi ndi zimene mukundipatsa monga mphoto yanga? Ngati mukundipatsa zimenezi, ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+
6 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti Gaza wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anthu onse ogwidwa ukapolo+ anawapereka ku Edomu.+
4 Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,+ ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+ Kunena za Asidodi,+ anthu ake adzawathamangitsa dzuwa lili paliwombo,+ ndipo Ekironi adzazulidwa.+
5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha. Gaza adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitikiranso Ekironi+ chifukwa chakuti amene anali kumudalira+ adzachita manyazi. Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu ndipo m’dziko la Asikeloni simudzakhalanso anthu.+