2 Mafumu 19:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Atentha milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga. Salimo 115:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+ Yeremiya 10:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+ Yeremiya 16:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Kodi munthu wochokera kufumbi angapange milungu? Zimene munthu amapangazo si milungu yeniyeni.+ 1 Akorinto 8:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+
18 Atentha milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga.
5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+
4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+