11 Kodi pali mtundu wa anthu umene unasinthanitsapo milungu yawo+ ndi zinthu zimene kwa iwo si milungu yeniyeni?+ Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zosapindulitsa.+
26 Tsopano mukuona ndipo mukumva za Paulo ameneyu, kuti si mu Efeso+ mokha muno mmene wakopa anthu ambirimbiri ndi kuwapatutsira ku chikhulupiriro china. Wachita zimenezi pafupifupi m’chigawo chonse cha Asia. Iye akumanena kuti milungu yopangidwa ndi manja+ si milungu ayi.
4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+