Yesaya 23:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Yehova wa makamu ndi amene wapereka chigamulo chimenechi,+ kuti anyansitse kukongola kwa mzindawo ndi kuchotsa kunyada kwake,+ ndiponso kuti anyoze anthu onse olemekezeka a padziko lapansi.+ Yeremiya 9:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Yehova wanena kuti: “Munthu wanzeru asadzitamande chifukwa cha nzeru zake.+ Munthu wamphamvu asadzitamande chifukwa cha mphamvu zake.+ Munthu wachuma asadzitamande chifukwa cha chuma chake.”+ Yeremiya 48:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 “‘Tsoka iwe Mowabu!+ Anthu a Kemosi+ awonongedwa. Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.
9 Yehova wa makamu ndi amene wapereka chigamulo chimenechi,+ kuti anyansitse kukongola kwa mzindawo ndi kuchotsa kunyada kwake,+ ndiponso kuti anyoze anthu onse olemekezeka a padziko lapansi.+
23 Yehova wanena kuti: “Munthu wanzeru asadzitamande chifukwa cha nzeru zake.+ Munthu wamphamvu asadzitamande chifukwa cha mphamvu zake.+ Munthu wachuma asadzitamande chifukwa cha chuma chake.”+
46 “‘Tsoka iwe Mowabu!+ Anthu a Kemosi+ awonongedwa. Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.