24 Kenako mfumu ya Asuri inatenga anthu kuchokera ku Babulo,+ Kuta, Ava,+ Hamati,+ ndi Sefaravaimu+ n’kuwakhazika m’mizinda ya Samariya,+ m’malo mwa ana a Isiraeli. Anthuwo anatenga Samariya n’kumakhala m’mizinda yake.
12 “Yehova akadzatsiriza ntchito yake yonse m’phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu, ndidzalanga mfumu ya Asuri chifukwa cha zipatso za mwano wa mumtima mwake ndiponso chifukwa cha kudzikuza kwa maso ake onyada.+
18 “Abusa ako ayamba kuwodzera,+ iwe mfumu ya Asuri, ndipo anthu ako olemekezeka akungokhala m’nyumba zawo.+ Anthu ako amwazikana pamapiri ndipo palibe amene akuwasonkhanitsa pamodzi.+