-
2 Mafumu 22:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 “Pitani mukafunse+ kwa Yehova m’malo mwa ineyo, m’malo mwa anthuwa, ndi m’malo mwa Yuda yense. Mukafunse zokhudza mawu a m’buku limene lapezekali, chifukwa mkwiyo wa Yehova+ umene watiyakira ndi waukulu, popeza makolo+ athu sanamvere mawu a m’buku ili. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.”+
-
-
Ezekieli 20:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 “‘“Koma iwowo, a nyumba ya Isiraeli, anandipandukira m’chipululu.+ Iwo sanayende motsatira malamulo anga+ ndipo anakana zigamulo zanga+ zimene munthu akamazitsatira, amakhala ndi moyo.+ Sabata langa analidetsa kwambiri,+ moti ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga m’chipululu kuti ndiwafafanize.+
-