Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu,+ kuti uzule, ugwetse,+ uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kubzala.”+

  • Yeremiya 12:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Yehova wanena kuti: “Anthu onse oipa amene ndinayandikana nawo + amene akukhudza cholowa chimene ndinapatsa anthu anga Aisiraeli kuti chikhale chawo,+ ndikuwazula pamalo awo.+ Ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pawo.+

  • Yeremiya 25:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ watero Yehova, “ndipo ndikuitananso Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mtumiki wanga.+ Ndikuitana anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu okhala mmenemo, komanso kuti aukire mitundu yonse yokuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani, ndi kukusandutsani chinthu chodabwitsa chimene azidzachiimbira mluzu+ ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.+

  • Yeremiya 45:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Umuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Taona! Zimene ndamanga, ndikuzigwetsa, ndipo zimene ndabzala, ndikuzizula. Ndichita zimenezi m’dziko lonse.+

  • Amosi 9:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyang’ana ufumu wochimwawo,+ ndipo ndidzaufafaniza panthaka ya dziko lapansi.+ Komabe nyumba ya Yakobo+ sindidzaifafaniza yonse.

  • Yona 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako Yona analowa mumzindawo ndi kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye anali kulalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena