4 Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati chitsamba chaminga, ndipo munthu wowongoka mtima kwambiri pakati pawo ndi woipa kwambiri kuposa mpanda wa mitengo yaminga.+ Tsiku limene mudzapatsidwe chilango, limene alonda anu ananena, lidzafika ndithu.+ Pa tsikulo anthu adzathedwa nzeru.+