Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu,+ kuti uzule, ugwetse,+ uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kubzala.”+

  • Yeremiya 4:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Udzalipira chifukwa cha khalidwe lako ndi zochita zako.+ Limeneli ndilo tsoka lako chifukwa zidzakhala zowawa. Zidzatero chifukwa kupanduka kwako kwalowerera mpaka mumtima.”

  • Yeremiya 5:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndiyeno mudzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu watichitira zonsezi?’+ Pamenepo ukawayankhe kuti, ‘Popeza mwandisiya ine Mulungu wanu ndipo mwapita kukatumikira mulungu wachilendo m’dziko lanu, mudzatumikiranso alendo m’dziko limene si lanu.’”+

  • Yeremiya 11:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Yehova wa makamu, Wokubzalani,+ wanena kuti tsoka lidzakugwerani chifukwa cha zoipa zimene a m’nyumba ya Isiraeli+ ndi a m’nyumba ya Yuda achita ndi kundikhumudwitsa nazo pofukizira Baala nsembe zautsi.”+

  • Yeremiya 21:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “‘“Mzinda uwu ndaukana* ndipo ukumana ndi tsoka osati zabwino,”+ watero Yehova. “Ndidzaupereka m’manja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo idzautentha ndi moto.”+

  • Yeremiya 31:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “Monga mmene ndakhalira ndikufunafuna mpata+ kuti ndiwazule, kuwagwetsa, kuwapasula, kuwawononga ndi kuwasakaza,+ ndidzakhalanso nawo tcheru kuti ndiwamange ndi kuwabzala,”+ watero Yehova.

  • Ezekieli 7:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Mapeto akubwera,+ ali m’njira. Akufikira mwadzidzidzi. Akubwera ndithu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena