Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 25:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova Mulungu wa Isiraeli anandiuza kuti: “Landira chikho ichi chimene chili m’dzanja langa. Mmenemu muli vinyo wa mkwiyo ndipo ukamwetse mitundu yonse imene ndikukutumizako.+

  • Yeremiya 25:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho ndinatenga chikho chija chimene chinali m’dzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako.+

  • Yeremiya 25:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ngati angakakane kulandira chikhochi m’manja mwako kuti amwe ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mumwabe basi.+

  • Maliro 4:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Kondwa ndipo usangalale,+ iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala m’dziko la Uzi.+

      Iwenso kapuyo ikupeza.+ Udzaledzera ndipo anthu adzakuona uli maliseche.+

  • Obadiya 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Pakuti mmene anthu inu munali kumwera vinyo paphiri langa loyera, ndi mmenenso mitundu ina yonse ya anthu izidzamwera mkwiyo wanga ngati vinyo nthawi zonse.+ Iwo adzamwa ndi kugugudiza mkwiyo wanga, ndipo zidzakhala ngati iwo kunalibe.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena