Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 20:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Koma Yehova anali nane+ ngati msilikali wamphamvu ndi woopsa.+ N’chifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana.+ Adzachita manyazi kwambiri chifukwa adzaona kuti sizinawayendere bwino. Manyazi awo adzakhala nawo mpaka kalekale ndipo sadzaiwalika.+

  • Ezekieli 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma ndachititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo,+ ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo.+

  • Mika 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma ine ndili ndi mphamvu zochuluka chifukwa cha mzimu wa Yehova. Ndine wokonzeka kuchita zachilungamo ndi kusonyeza mphamvu+ kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kupanduka kwawo, komanso kuti ndiuze Isiraeli za tchimo lake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena