Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 25:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mneneriyo atangonena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Siya kunena zimenezi.+ Kodi ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndithu ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kuti akuwonongeni+ chifukwa cha zimene mwachitazi,+ ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+

  • Miyambo 29:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Munthu wodzudzulidwa kawirikawiri+ koma amene amaumitsa khosi lake,+ adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo akadzatero sadzachira.+

  • Yeremiya 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Koma anthu inu ndinakuutsirani alonda+ ndipo ndinati, ‘Mverani kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa!’”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitidzamvera.”+

  • Zekariya 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “‘Musakhale ngati makolo anu+ amene aneneri akale anawauza mofuula+ kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine!’”’+

      “‘Koma iwo sanamvere ndipo sanalabadire mawu anga,’+ watero Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena