3Ine ndinapitiriza kunena kuti: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo ndi inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi si inu oyenera kudziwa chilungamo?+
17 Tsoka m’busa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+ Lupanga lidzamutema padzanja ndi kuboola diso lake la kudzanja lamanja. Dzanja lake lidzafota,+ ndipo diso lake la kudzanja lamanja lidzachita mdima.”