-
2 Mafumu 23:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kenako inaitanitsa ansembe onse kuchokera m’mizinda ya Yuda. Inawaitanitsa kuti isandutse malo okwezeka kukhala osayenera kulambirako, kumene ansembewo ankafukizako nsembe yautsi, kuyambira ku Geba+ mpaka ku Beere-seba.+ Inagwetsa malo okwezeka a pazipata amene anali pakhomo la pachipata cha Yoswa mkulu wa mzindawo. Chipata cha Yoswacho chinali mbali ya kumanzere munthu akamalowa pachipata cha mzindawo.
-