Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Danieli 7:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Idzalankhula mawu otsutsana ndi Wam’mwambamwamba+ ndipo idzazunza mosalekeza oyera a Wamkulukulu.+ Idzafuna kusintha nthawi+ ndiponso lamulo+ ndipo oyerawo adzaperekedwa m’manja mwake kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi.+

  • Danieli 12:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamenepo ndinamva mwamuna wovala nsalu uja, amene anaimirira pamwamba pa madzi a mumtsinje akuyankha. Poyankhapo, anakweza m’mwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere ndi kulumbira+ pa Iye amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzapita nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu, ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.+ Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya+ mphamvu za anthu oyera, zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”

  • Luka 21:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu+ za anthu a mitundu inawo zitakwanira.

  • Chivumbulutso 12:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri+ a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu,+ kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa+ kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi njoka ija.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena